Theresa Phondo & Kelvin Sings - Assurance (Visualizer)

Описание к видео Theresa Phondo & Kelvin Sings - Assurance (Visualizer)

Zaka zambiri zatha
Iwe ine tikucheza
Mphekesela zinkamveka kuti ife ndi chibwenzi
Koma ife tinkakana
Timvekere sizingatheke
Iwe ndi ine sitilola

Lero ndatopa ndi mafunso
Omadzifunsa ndekha
Ine ndalema ndi mafunso
Ondifusanso ena
Chifukwa chomwe ndimadziwa
Nchoti ndimakukonda
Chimodzi chomwe n’funa n’dziwe
Ndimve pakamwa pako

Ngati umandikondadi ine
Umandifunadi ine
Ndimafuna ndidziwe
Ndidziwe ndidziwe
Ndimafuna ndidziwe
Ndidziwe ndidziwe

Nthawi nde ikupita
Nkhawa nde zikubwerabe (bwerabe)
Chovuta kodi nchani
Kunena m’mene umamvera yeah
I need some assurance
Munthune ndikukula yeah
Nde tangonena
Tipange mapulani
Kuti zinthu zikhala bwanji

Poti ndatopa ndimafunso
Omadzifunsa ndekha
Ine ndalema ndimafunso
Ondifusanso ena

Ooh chifukwa chomwe ndimadziwa
Iwe ndiamene ndimakonda
Chimodzi chomwe n’funa n’dziwe
Ndimve pakamwa pako

Kodi umandikondadi iwe
Oooh umandifunadi iwe
Ndimafuna ndidziwe
Ndidziwe ndidziwe
Ndimafuna ndidziwe
Ndidziwe ndidziwe

Ooohhh umandikondadi iwe
Umandikondadi iwe
Ndimafuna ndidziwe
Ndidziwe ndidziwe
Ndimafuna ndidziwe
Ndidziwe ndidziwe

Ndidziwe ndidziwe ndidziwe
Patseko assurance

Ndimafuna ndidziwe ndidziwe ndidziwe
Munthune ndikukula

Ndidziwe ndidziwe ndidziwe
Patseko assurance, munthune ndikukula

Ndimafuna ndidziwe ndidziwe ndidziwe
Patseko assurance, munthune ndikukula

Комментарии

Информация по комментариям в разработке